Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Chitukuko chifalikira m’boma lonse la Nsanje — Zikhale

Nduna ya za m’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, yalonjeza anthu ku Nsanje kuti boma lipitilira kukhazikitsa ntchito za chitukuko m’bomali ndi cholinga chotukula bizinesi zawo.

Poyankhula pa msonkhano wa chitukuko pa bwalo la Mpatsa CDSS mdera la pakati m’boma la Nsanje, a Zikhale Ng’oma, omwenso ndi mkulu okonza mapulani m’chipani cha MCP, ati ichi ndi chifukwa boma layika chidwi pobwezeretsa maulendo a njanji olumikiza bomali ndi maboma ena komanso dziko la Mozambique.

Pamsonkhanowo, a Ng’oma alandira anthu 300 ochoka ku chipani chotsutsa cha DPP kulowa MCP.

Related posts

Mwambo wachionetsero cha zokopa alendo wayamba

Romeo Umali

‘Boma likukumana ndi zovuta polimbana ndi mchitidwe wa nkhanza kwa anthu achikulire’

Rabson Kondowe

UTM yapempha mgwirizano pa nthawi ya maliro

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.