Inkosi ya Makosi Gomani V ya m’boma la Ntcheu yati ili ndi chisoni chachikulu kaamba ka imfa ya Impi Bhiyeni Dr Saulos Chilima.
Inkosiyi yati Dr. Chilima anali mlangizi wa chingoni amene amamukonda, ndipo anali olimbikira, odzipereka ndi olimbikitsa chikhalidwe komanso odzipereka ku mpingo.
Iwo anayamikiranso khwimbi la anthu amene akupereka ulemu wawo otsiriza kwa malemu Dr. Chilima.
Koma iwo anati ngakhale aMalawi ali pa chisoni chachikulu, akuyenera kulimbikitsa mtendere.
Inkosi Ya Makosi Gomani yalangizanso aMalawi kuchita ndale zokomera dziko lonse.