Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Akubanja ayamikira boma powonesa chikondi mu nthawi ya zobvutayi

Oyimira akubanja kwa mayi Mary Chilima, bambo Ziliro Chiwambo, anati akuyamika mtsogoleri wa dziko lino  komanso aMalawi chifukwa cha chikondi chomwe aonetsa pa zovutazi.

Iwo anati imfa ya Dr. Chilima yawakhudza kwambiri chifukwa ataya munthu amene anali mzati.

Iwo anati nkofunika kuti a Malawi aonetsetse kuti akutsatira zomwe Dr. Chilima amachita kumtundu wa aMalawi.

Iwo anati Dr.Chilima anali ndi mtima wodzichepetsa komanso okonda mtendere.

M’mau awo, a Rose Kamoto poyimiranso akubanja kuchokera kwa mfumu Likoswe m’boma la Chiradzulu, anabwerezanso kuti malemu Dr Chilima anali munthu wodzichepetsa kwambiri.

Iwo anapitiliza kuyamika boma komanso mpingo chifukwa chathandizo lomwe apereka m’magawo osiyanasiyana.

A Ben Chilima, omwe anaimila akubanja la a Chilima, anathokoza anthu osiyanasiyana omwe athandiza pa zovuta za achimwene awo.

Iwo anati akubanja la a Chilima apempha boma kudzera kwa a Prezidenti kuti ngati nkotheka, mtsogolo muno adzamange malo achikumbutso ku Chikangawa pokumbukira Malemu Dr Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu amene amwalira pangozi ya ndege lolemba sabata latha.

Related posts

Baylor College of Medicine tackles health sector gaps through research

Romeo Umali

Kaunda involved in motorcycle accident

Romeo Umali

Experts criticise Malawi Queens’ performance at 2025 Africa Netball Cup

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.