Thupi la wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, malemu Dr Saulos Chilima, aliyika m’manda pamudzi wa Mbirimtengelenji pa Nsipe m’dera la Senior Chief Inkosi Champiti m’boma la Ntcheu.
Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ndi amene anatsogolera aMalawi pamwambo oyika malemu Dr. Chilima m’manda.
Asilikali a Malawi Defence Force anaomba mizinga khumi, isanu ndi inayi popereka ulemu wawo otsiliza kwa malemuwa.
Dr Chakwera ndi mayi Monica Chakwera anakayalanso nkhata pa mwambowu.
Wamkulu wa asilikali, a nkhondo General Paul Valentino Phiri pamodzi ndi wamkulu wa apolisi, a Merlyne Yolamu, onse anakapereka nawo ulemu otsiriza.
Atsogoleri akale a dziko lino, Dr Bakili Muluzi ndi Professor Peter Mutharika pamodzi ndi mayi Getrude Mutharika, anakapelekanso ulemu otsiriza.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wopuma, a Khumbo Hastings Kachali, Chief Justice Rizine Mzikamanda, mlembi wamkulu mu ofesi ya Prezidenti ndi Kabineti komanso nduna za boma mwa ena ambiri, nawonso anachita motero.