Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

Medina Stars yatenga chikho cha Zikhale ku Nkhata Bay

Timu ya Medina Stars yatenga chikho cha Ken Zikhale Ng’oma chimene ndi cha ndalama zokwana K6 million itagonjetsa timu ya Hauten 5-1 Lamulungu masana ku Tukombo m’boma la Nkhata Bay.

Zateremu, Medina yalandira K1.2 million pamene Hauten yalandira K600,000. Timu iliyonse imene inatenga gawo mu mpikisanowu yalandira kangachepe motengera ndi mmene yamalizira mu mpikisanowo, ngati chipukuta misozi.

Ku masewero a mpira wa manja (Netball), timu ya Brazil Sisters yapambana itagonjetsa Tukombo Sisters ndi zigoli 40 kwa 29 ndipo yalandira ndalama zokwana K600,000.

Nawonso matimu amene anatenga nawo gawo mu mpikisanowu alandira kangachepe.

A Zikhale Ng’oma anati ndi okhutira ndi mmene zayendera mu mpikisanowo chifukwa osewera awonetsa luso limene matimu akukuakulu angathe kudzapeza, maka achinyamata achisodzera.

Iwo ndi phungu wa chipani cha Malawi Congress ndipo amayimira dera la kummwera kwa boma la Nkhatabay komanso ndi nduna yoona za chitetezo cha m’dziko.

Olemba: Hassan Phiri

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tumaini Festival gears up for 10th anniversary celebration with fundraiser

Yamikani Simutowe

Malawi nears completion of environment report after 15-year gap

McDonald Chiwayula

M’mbelwa DC urges community to utilise funds prudently

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.