Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Ndabwera ndi nyimbo zotonthoza mitima-watero Levysai Kalepa

Katswiri oyimba nyimbo zauzimu Levysai Kalepa yemwe amakhala ku England koma ndi nzika ya dziko lino wati waganiza zodzatumikira ku Malawi pofuna kupereka mpata kwa a Malawi kuti asangalare ndi nyimbo zake zomwe wati anazikhazikitsa kale mu mzinda wa Manchester ku England.

Kalepa wafika mdziko muno pomwe akuyembekezeka kukhala ndi mwambo wamaimbidwe ku Blantyre, Lilongwe komanso ku Mchinji mwezi uno.

“Nyimbo zanga zili ndi uthenga otonthoza omwe akulira, olimbikitsa ofooka, opeleka chipembedzo kwa omwe akuona ngati alibe kolowera komanso osangalatsa,” Kalepa anatero.

M’modzi mwa oyimba nyimbo zauzimu mdziko muno Norman Phiri wati iye limodzi ndi oyimba ambiri mdziko muno athandizana naye Kalepa kuti cholinga chake chikwaniritsidwe.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Aphungu awiri a DPP agwirana pakhosi

MBC Online

Alexander ‘Cage’ Likande wamwalira

Foster Maulidi

A Likhutcha alimbikitsa bata

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.