Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Banja lina alimanga litaba mwana ku chipatala

Apolisi ku Lilongwe amanga Wyson Misoya ndi mkazi wake Gloria onse azaka 32 powaganizira kuti aba mwana wamasiku awiri pa chipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe.

Mneneri wapolisi ku Lilongwe Hastings Chigalu wati awiriwa anakwatirana chaka cha 2022 ndipo mwamunayo wakhala akuumiriza mkazi wakeyo kuti amubekere mwana.

Kenako mkaziyo ananamizira kuti ndiwoyembekezera ndipo awiriwo anapita ku chipatala cha Bwaila. Atawona kuti alephera kuba mwana pachipatalacho, iwo anapita pachipatala cha Kamuzu Central.

Kumeneko mkaziyo anauza mayi wina yemwe ananyamula mwana kuti amulandire ndipo anathawa naye. Koma amayi ena amene amakhala pafupi ndi banjali anakanena ku polisi kamba koti anadabwa kuti banjali liri ndi mwana pomwe mkazi wa mnyumbamo sanali woyembekezera.

Wyson Misoya ndi wa mmudzi wa Mwabvi mfumu yaikulu Nsabwe ku Thyolo, pomwe Gloria Misoya ndi wa mmudzi wa Denyama mfumu yaikulu Ntchema ku Chiradzulu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Promise Kamwendo wapepesa!

Romeo Umali

Timu ya Draughts yalephera kupita ku Russia

MBC Online

Lingadzi Police arrests hacker

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.