Kampani yogulitsa gas ya 265 Energy Limited yalimbikitsa ochita malonda kuti atsegule nthambi zawo mmaboma a m’dziko muno kuti anthu azipeza gasi mosavuta.
Wofalitsa nkhani za kampaniyi, a Phillip White, anena izi pomwe atsegula nthambi posachedwapa ku Mzuzu.
Pogwirizana ndi zomwe a White anena, a Biliati Lifuletu aku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe, omwe ndi mmodzi mwa anthu omwe amagwiritsa ntchito gas, ati kupezeka kwa gas mosavuta pa msika kutha kuthandiza kuthana ndi vuto losakaza nkhalango pomatentha makala.
Unduna woona zamphamvu za magetsi ukulimbikitsa ubale ndi kampani zomwe zimagulitsa zipangizo zamphamvu zamagetsi zomwe siziononga chilengedwe.