Bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority MRA lati likukumana ndi mavuto pa ntchito yotolera misonkho, maka pa galimoto zimene zimalowa m’dziko muno mozemba.
Mkulu wazamalonda ku bungweli, a Wilma Chalulu, wati anthu ena samafuna kuti galimoto zawo azifufuze ngati analipira msonkho kapena ayi polowa m’dziko muno.
A Chalulu apempha olembankhani kuti athandize kudziwitsa anthu zakufunika kopereka msonkho pa galimoto polowa mdziko muno komanso kupereka mpata ku bungweli kugwira ntchito mosavuta yofufuza galimoto zamtunduwu.
Boma limagwiritsa misonkho munjira zosiyanasiyana monga kumanga misewu, sukulu, zipatala, nyumba za ogwira ntchito m’boma komanso kupereka malipiro awo.