Prezidenti wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera watsimikizira anthu m’boma la Dowa kuti ntchito yopopa madzi m’nyanja ya Malawi ithandiza kubweretsa ukhondo ndi madzi pafupi kwa anthu m’bomalo.
Iye wati ntchitoyo yayamba kale ndipo akuyigwira ndi a kampani ya Khatho Civils ndipo idzapatutsa madziwo kuti nawo anthu ku Dowa athandizike.
Pa ntchito zina zachitukuko, Dr Chakwera wati boma lake lamanga kale nyumba 50 za asilikali aku Support Battalion ya MDF ku Mvera, kufikitsa magetsi a MAREP kumidzi, komanso anati boma likulingalira zopaka phula msewu wapakati pa Mvera ndiku Nalunga m’boma la Dowa.
Mtsogoleri wa dziko linoyu analimbikitsa achinyamata kuti apeze ngongole ya NEEF kuti bizinesi ndi ulimi wawo zipite patsogolo.
Phungu waderalo, a Richard Chimwendo Banda komanso Inkosi Chiwere, ati anthu a mderalo alembetsa kale mwaunyunji pokonzekera chisankho cha 2025.
By Isaac Jali