Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani Politics

Msonkhano waukulu wa PP wayamba

Msonkhano waukulu wa chipani cha People’s (PP) wayamba munzinda wa Lilongwe, komwe nthumwi za chipanichi zoposa 1000 zisankhe adindo atsopano.

Wapampando wa komiti yomwe yakonza msokhanowu, a Peter Kamange, wati PP imalemekeza nfundo komanso nsanamira za demokale, ndi chifukwa chake amakonza msokhanowu, womwe umapereka mwayi kwa otsatira chipanichi kusankha adindo.

Mmodzi mwa akuluakulu a PP a Ben Chikhame ati akatsiriza msonkhanowu, ayamba ntchito yokonza manifesto omwe akhale akulumikizana ndi mfundo komanso masomphenya achitukuko a Malawi 2063.

Pamsonkhanowu pafikanso nthumwi zoimira ma ofesi a kazembe a maiko a America, Britain, Norway, komanso mgwirizano wa maiko aku ulaya (EU). Nalo bungwe la Oxfam, lomwe limalimbikitsa amayi kuchita nawo ndale, latumiza nthumwi zake.

Zokambirana pamsokhanowu zikhazikika pa mutu womwe pachingerezi akuti Restoring the Hope: Building a Brighter Future Together.

Olemba: Yamikani Simutowe

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Akabaza kalembetseni m’kaundula wa voti’

Emmanuel Chikonso

Burning Spear wapereka mphatso ya gitala kwa President Chakwera

MBC Online

Mtukula pakhomo wammizinda walowa

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.