Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Phindu la Illovo latsika mu miyezi isanu ndi umodzi

Phindu la kampani ya Illovo Sugar Malawi latsika kufika pa K32.5 billion mu miyezi ya pakati pa September chaka chatha mpaka February chaka chino, kuchoka pa K48.6 billion miyezi ngati yomweyi mu 2023 ndi 2024.

Izi ndi malinga ndi uthenga wa m’mene chuma cha kampaniyi chayendera mu miyezi isanu ndi umodzi ya chaka chake cha chuma omwe wasayinidwa ndi mkulu wa kampaniyi,  a Lekani Katandula,

komanso wampando wa bodi, a Jimmy Lipunga.

Illovo yati izi zachitika kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, kuphatikizapo kuti ulimi wa nzimbe sunayende bwino mu nthawiyi chifukwa cha namondwe komanso kubedwa kwa nzimbe ndi katundu wa kampaniyi, mwazina.

Pa chifukwa ichi, anthu amene ali ndi masheya mu Illovo sapatsidwa gawo la phinduli (dividend).

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FISCAL POLICE NAB MULLI, MUHARA

MBC Online

Chakwera Calls for Robust Regional Integration

Alick Sambo

Takhumudwa posawasankha a Navicha – NGOGCN

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.