Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lati achinyamata sakubweza ngongole za bungweli moyenera akayerekeza ndi magulu ena amene akutenga ngongolezi.
Wapampando wa board ya bungweli, a Jephta Mtema, ndi amene ayankhula izi pa msonkhano umene bungweli linakonzera atsogoleri osiyanasiyana a munzinda wa Mzuzu ofotokoza mmene ngongoleyi ikuyendera.
Iwo ati achinyamata ambiri amakhala asanakhazikike muzochitika akamatenga ngongolezi ndipo nthawi yobweza amakhala kuti anasiya malonda komanso akuchita zina.
A Mtema ati achinyamata ena amakhala kuti alibe ukadaulo oyenereka oyendetsa malonda akamatenga ngongolezi ndipo amakhala akuphunzilira pa ngongoleyi.
Mfumu ya mzinda wa Mzuzu, a Kondwani Nyasulu, anati ngongole ya NEEF ili ndi kuthera kosintha miyoyo ya anthu akayigwiritsa bwino ntchito.
Olemba: Henry Haukeya