Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Anthu ochuluka asonkhana ku maliro a Hope Chisanu

Mwambo wa maliro a malemu Hope Chisanu watsala pang’ono kuyamba m’mudzi wa Nyaka, mdera la mfumu yayikulu Kalumbu, m’boma la Lilongwe.

A Chisanu adamwalira pa 1 June m’dziko la USA kumene amakhala ndipo thupi lawo lafika m’dziko muno lachiwiri lapitali.

Iwo adagwirapo ntchito ku wayilesi ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) kumene adatchuka ndi dzina lakuti ‘Uncle Bembelezi’ ndipo adadziwikanso ndi zisudzo akamachita sewero ndi gulu la Wakhumbata Ensemble Theatre.

Iwo amachita nawo sewero la Theatre of the Air lomwe limawuluka pa wailesi ya MBC Radio 1.

Olemba: Isaac Jali

Related posts

Airtel Africa expresses commitment towards improving teachers’ lives

MBC Online

UK-based Malawian striker making strides

Romeo Umali

Thandizani boma pothetsa katangale — Chimwendo Banda

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.