Chiwerengero cha anthu omwe amwalira atamwa mowa odziwika kuti ‘ambuye tengeni’ kwa Manase ku Blantyre tsopano chafika pa asanu ndi atatu 8.
Apolisi atsimikiza kuti amanga anthu atatu kamba kankhaniyi.
MBC itatsatira nkhaniyi lero yapezanso kuti anthu ena awiri ali mwakayakaya pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth pomwe munthu mmodzi amutulutsa atachira.