Apolisi munzinda wa Lilongwe amanga a Justin Mataka, 27, powaganizira kuti anaba makina opimira amayi oyembekezera pa chipatala cha Bwaila.
A Mataka, amene anayamba kugwira ntchito yothandizira pa chipatalachi chaka chatha, akayankha mlandu wa kuba pantchito kubwalo lamilandu Lolemba likudzali.
Makinawo ndi a K6 million ndipo a Makata adakawagulitsa ku chipatala china chimene sichaboma munzindawu pa mtengo wa K2 million ndipo anali atalandira kale K1.8 million.
Ofalitsankhani za polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, anati mlanduwo unachitika Lachinayi pa 16 January 2025.
A Chigalu ati amene akuwaganizirawa anawagwira atadziwa kuti munthu amene anazembetsa katunduyo analowa m’chipinda chimene amasunga makinawo pogwiritsa ntchito kiyi amene anakonzetsa yekha.
Wakubayo anavomera mlanduwu ndi kulondolera apolisi kuchipatala china chimene sichabomacho kumene anagulitsa makinawa.
Mataka ndi wa m’mudzi wa Makuta mdera la mfumu yayikulu Malengachanzi m’boma la Nkhotakota.