Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Akhale atachoka pasanathe masiku khumi ndi anayi – Unduna waza malonda

Unduna waza malonda ndi mafakitale walamula kuti m’mwenye yemwe anatsekula shopu yake  ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe, momwe amagulitsa zinthu za hardware, akhale atatseka shopu yake pasanathe masiku 14.

Malinga ndi chikalata chomwe wasayinila m’modzi mwa akuluakulu ku unduna waza malonda, a Ezron Chirambo, m’mwenyeyu sakuyenera kuchita bizinesi yake kumsika wa Nsungwi.

Masiku apitawa, mavenda wogulitsa zinthu za hardware ku Nsungwi anatseka sitolo ya m’mwenyeyu pokwiya naye kamba koti amasokoneza malonda awo chifuwa  mpamba wawo sukugwirizana ndi mapezedwe am’mwenyeyo, yemwe akuti amaphangira bizinesi pogulitsa mwachipiku komanso pang’onopang’ono katundu yemwe amapanga yekha.

Prezidenti wabungwe la Black indigenous business Network a Kate Kamwangala ati zomwe boma lachita pa nkhaniyi zaonetsa kudzipereka kwake polimbikitsa a bizinesi zing’ono zing’ono mdziko muno.

M’neneli wa mavenda aku Nsungwi, a Albert Zuwawo, wayamika boma chifukwa choonetsetsa kuti abizinesi zing’ono zing’ono m’dziko muno sakuphinjika.

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

Minister of Gender advocates for local skilled labour in smart lab projects

MBC Online

Dedza DEST urged to be professional ahead of 2025 polls

MBC Online

Chakwera graces World Creativity & Innovation Day

Eunice Ndhlovu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.