Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, wati ndi udindo wa akuluakulu a boma, kuphatikizapo aku unduna oona zachilengedwe ndi kusintha kwa nyengo, kuchilimika polondoloza malonjezo a zachuma kuchokera ku maiko olemera pa msonkhano waukulu wa COP 29, umene uchitikire mdziko la Azerbaijan kuyambira pa 11 kufika pa 22 November.
Polankhula pakutha kwa msonkhano wamasiku awiri wa akuluakulu a boma, omwenso unali wokonzekera za msonkhano waukuluwu, Dr Usi anati nthawi yakwana yoti wina aliyense wokhudzidwa adzalankhule mwachindunji pofuna kuti maiko olemera akwaniritse malonjezo awo omwe adachita pa nkhani ya thandizo la ndalama zopita ku maiko ongokwera kumene, omwe akhudzidwa komanso kuvutika kwambiri ndi kusintha kwa nyengo.
Mmawu ake, mmodzi mwa akuluakulu a dziko la Azerbaijan, a Yalchin Rafiyev, anati dziko lawo lakonzeka kudzachititsa msonkhano waukuluwu, omwenso udzabweretse zotsatira zokomera maiko okwera kumene, kuphatikizapo la Malawi.
Dr Usi anyamuka laMulungu lino kuchokera ku Azerbaijan kubwelera ku Malawi.