Kampani yopanga sugar ya Illovo yakonza ntchito zosiyanasiyana zofuna kutolera ndalama zothandizira ukhondo wa atsikana msukulu zina zamdziko muno.
Izi zikuchitika pansi pantchito ya Rise for Girls yomwe mwazina idzithandiza kupeza zipangizo za ukhondo zogwiritsira ntchito atsikanawa panthawi ya msambo.
Illovo yati yayika kale ndalama zokwana K100 miliyoni muntchitoyi ndipo ipitiriza kufunafunaso ndalama zina ndicholinga choti ntchitoyi ifikire atsikana ambiri.
Mmawa wa Loweluka kampaniyi inachititsa masewero a Golf ku Kasasa Golf Club m’boma la Nkhotakota pofuna kupeza ndalamazi.
Pakali pano, madyerero amgonero omwe akonza m’mbomali ngati njira imodzi yofuna kupeza ndalamazi ali mkati.