Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wayatsa magetsi pa sitolo za Luviri m’boma la Mzimba muntchito yopereka magetsi akumudzi ya MAREP.
Luviri ndi imodzi mwa ma trading centre 13 amene akulandira magetsi mu ntchito yachisanu ndi chinayi (9) yopereka magetsi kumidzi.
Pakadali pano, mabanja okwana 50 mwa 250 omwe anayerekeza kuti apeza magetsiwa alandira kale kuderali.
Malinga ndi nduna yowona za mphamvu za magetsi, a Ibrahim Matola, boma lapeza ndalama zoposa €70 million zomwe zithandizire kuika mapolo achitsulo kuchoka ku Nkhoma Power Station ku Lilongwe kufika m’chigawo cha kumpoto.
Dr Chakwera, amene ali pa ulendo opita ku chigawo cha kumpoto, anaima kucheza ndi anthu amene anali mu njira, kudikilira kuti awaone.