Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News Nkhani

‘Ngongole za NEEF ndiza aliyense’

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, wati zokambirana zomwe bungwe la NEEF likuchita ndi anthu zikuthandiza kuti anthu amvetse ndikutsatira momwe ngongole ya bungweli ikuyendera.

Dr Usi ayankhula izi pa zokambirana zomwe bungweli lachititsa ndi adindo a m’boma la Blantyre monga mafumu, makhansala, komanso ena mwa aphungu ochokera m’bomali.

Iwo ati ali ndi chiyembekezo kuti anthu oyenera ndiwo adzitenga ngongolezi ndipo anatsindika kuti ngongolezi sizandale koma za a Malawi.

Mkulu wa bungwe la NEEF, a Humphreys Mdyetseni, ati bungweli liri ndi mitundu ya ngongole yokwana 25 zomwe likupereka kwa anthu mdziko muno.

Ndipo mayi Mary Chikopa amene amachita bizinesi yogulitsa nsalu mu msika wa Limbe, ati iwo ndi m’modzi mwa anthu omwe apindula ndi ngongole ya NEEF ndipo ati buzinesi yawo yakula.

Mgawo loyamba la ngongole za NEEF, bungweli linapereka ndalama zokwana K100 billion ndipo posachedwapa, boma linakhazikitsa ndalama zokwana K350 billion zimene likupereka kwa anthu pothetsa umphawi.

Olemba: Mercy Zamawa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Demand quality products —MBS

MBC Online

CS-EPWP improving livelihoods of participants in Nkhata Bay

MBC Online

CHAKWERA EXPERIENCES MAKANJIRA ROAD’ ROUGH TERRAIN

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.