Apolisi ku Chiradzulu amanga John Tebulo wazaka 43 pomuganizira kuti wapha mwana wazaka zitatu kaamba kodutsa mmunda mwake.
Ofalitsankhani wapolisi ku Chiradzulu, Cosmas Kagulo, wati makolo a mwanayo analawilira kumunda kumusiya akugona kaamba koti mundawo unali pafupi.
Atadzuka, mwanayo anayamba kulondola makolo akewo ndipo anadutsira m’munda mwa Tebulo.
Izi sizinamusangalatse ndipo anatenga chikwanje ndikuyamba kukhapa mwanayo, yemwe anthu anathamangira naye kuchipatala koma mwatsoka, anali atamwalira.
Apolisi apulumutsanso woganiziridwayo kaamba koti anthu ammudzi anayamba kumumenya moti akulandira thandizo kuchipatala atavulala kwambiri.
Izi zachitika m’mudzi wa Likhomo, mfumu yaikulu Sandrack m’boma la Chiradzulu.
Olemba: Charles Pensulo