Phungu wadera lakumpoto m’boma la Kasungu, a Mike Bango, ayamika mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress, chifukwa choyambitsa ntchito yogawa chakudya kwa anthu amene akuvutika ndi njala m’boma la Kasungu.
A Bango, omwe amayankhula pa Nkhamenya Trading Centre m’bomalo, ayamikanso Prezidenti Chakwera chifukwa chokhazikitsa ntchito yomanga nyumba za achitetezo pa Nkhamenya komanso kwa Chatoloma.
Iwo anati ndi wokondwa kuti boma la Dr Chakwera laganizira zoonjezera chiwerengero cha anthu omwe akuyenera kupindula ku ntchito yogula zipangizo zaulimi zotsika mtengo.
Iwo anati anthu ambiri a m’boma la Kasungu ndi olemera chifukwa chakuyenda bwino kwa malonda a fodya ku msika.
Prezidenti Chakwera ali mboma la Kasungu kucheza ndi anthu pomwe akufotokozela mfundo zosiyanasiyana zachitukuko.