Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Takhumudwa posawasankha a Navicha – NGOGCN

Bungwe lolimbikitsa kuti amayi adzikhala m’maudindo akuluakulu la NGO Gender Cordination Network lati ladandaula kuti a Mary Navicha, omwe anali mtsogoleri wa aphungu a chipani cha DPP mnyumba ya malamulo  sanawasankhe kukhala mtsogoleri otsutsa boma m’nyumbayi. 

Wapampando wa bungweli, a Maggie Kathewera Banda, anena izi chipani cha DPP chitalengeza kuti chasankha a George Chaponda kukhala pa udindowu.

A Kathewera Banda ati iwo ndi anzawo akhala akuganiza kuti kaamba koti a Navicha akhala akugwirizira udindo otsogolera DPP mnyumba ya malamulo, komanso ngati njira yolimbikitsira amayi m’maudindo akuluakulu, amayenera kuwasankha kuti apitirize pa udindowu.

Akatswiri enanso a ndale monga a Chimwemwe Tsitsi komanso a Hawkins Munyenyembe, ati nawo amayembekezera kuti chipani cha DPP chisankha a Navicha chifukwa anaonetsa kale machawi popereka maganizo mosawopa ndi mosakondera pomwe amatsogolera aphungu a DPP mnyumba ya malamulo.

 

Olemba: Blessings Cheleuka

Related posts

Level 1 Hockey Coaching Course commences in Blantyre

Romeo Umali

Chakwera holds bilateral talks with Abu Dhabi Fund Director

Rabson Kondowe

Zokonzekera za Ku Mingoli zili mkati

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.