Mamembala ena a chipani cha UTM ati sakugwirizana ndi zotsatira zachisankho zimene zinachitika ku msonkhano waukulu wa chipanichi sabata yathayi.
Muzisankhozi, a Dalitso Kabambe ndi amene adawasankha kukhala mtsogoleri watsopano pamodzi ndi mamembala ena amene adawasankha maudindo osiyanasiyana.
Kusamvanaku kwadza pamenenso m’modzi mwa amene anapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa chipanichi, a Matthews Mtumbuka, anaganizirapo kuti chinyengo chinachitika kuti alephere.
Mu chikalata chimene atulutsa mamembalawa, ndipo asayinira ndi a Charles Kondowe, Kondwani Munthali ndi a Fletcher Katambalare, iwo ati ndi odabwa kuti anthu ena a chipani china anali nawo m’gulu la anthu ovota.
Iwo anatinso anthu onse amene anayambitsa nawo chipanichi sanapeze maudindo akuluakulu ndipo akuganizira kuti anthu ena amene ali m’maudindo atsopanowa anachita kuwatuma ndi a chipani china.
Gulu la anthuwa likugwirizana ndi zimene mtsogoleri wakale wa UTM, Dr Michael Usi, ananena kuti chipanichi sichinatsate ndondomeko zovomerezeka zochitira msonkhano waukulu.