Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ntchito yopopa madzi mu nyanja ya Malawi ichepetsa vuto la madzi ku Dowa – Chakwera

Prezidenti wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera watsimikizira anthu m’boma la Dowa kuti ntchito yopopa madzi m’nyanja ya Malawi ithandiza kubweretsa ukhondo ndi madzi pafupi kwa anthu m’bomalo.

Iye wati ntchitoyo yayamba kale ndipo akuyigwira ndi a kampani ya Khatho Civils ndipo idzapatutsa madziwo kuti nawo anthu ku Dowa athandizike.

Pa ntchito zina zachitukuko, Dr Chakwera wati boma lake lamanga kale nyumba 50 za asilikali aku Support Battalion ya MDF ku Mvera, kufikitsa magetsi a MAREP kumidzi,  komanso anati boma likulingalira zopaka phula msewu wapakati pa Mvera  ndiku Nalunga m’boma la Dowa.

Mtsogoleri wa dziko linoyu analimbikitsa achinyamata kuti apeze ngongole ya NEEF kuti bizinesi ndi ulimi wawo zipite patsogolo.

Phungu waderalo, a Richard Chimwendo Banda komanso Inkosi Chiwere, ati anthu a mderalo alembetsa kale mwaunyunji pokonzekera chisankho cha 2025.

 

By Isaac Jali

Related posts

President Chakwera to visit public projects

Romeo Umali

Iceland expands support for Home-Grown School Meals in Malawi

McDonald Chiwayula

MANEPO yayamikira Madam Chakwera polimbana ndi nkhanza za anthu achikulire

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.