Alimi omwe akuchita nawo ulimi wa mthilira wa minda ikuluikulu pa sikimu ya Mlambe Irrigation ku Mangochi, ayamikira bungwe la Green Belt Authority (GBA) kaamba kachidwi chomwe bungweli likuonetsa polimbikitsa ntchito za sikimuyi kuti zipindulire alimi ochuluka.
Wapampando wa gulu la alimiwa, Phillip Mkwela, alankhula izi ku Mangochi pamene bungwe la GBA limapereka ntchito ya gawo lachiwiri lokonzanso sikimuyi kwa akuluakulu a kampani ya Eistein Construction.
Kampani yatsopanoyi ikuyembekezeka kukonza malo ochuluka mahekitala 352 mugawo lachiwiri la ntchitoyi.
A Mkwera ati gawo lachiwiri la ntchitoyi likupereka chiyembekezo chachikulu choti alimiwa adzipeza phindu lochuluka.
M’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la GBA, a Synoden Kautsi, ati mwazina, kampani ya Eistein ikuyembekezeka kukonza ngalande zina zodutsa madzi, kuika magetsi oyendera mphamvu ya dzuwa, kupala ndi kukonza malo ochitira ulimi.
Malinga ndi a Kautsi, ntchitoyi yomwe ndi ya ndalama zokwana K21 billion, ikuyembekezeka kugwiridwa kwa miyezi isanu ndi inayi.
Mugawo loyamba, bungwe la GBA linakonza malo a ulimi okwana ma hekitala 48 pomwe alimi akolorapo chimanga chomwe analima.
Olemba: Owen Mavula