Oyendetsa ndi kukonza Ku Mingoli Bash, a Sound Addicts Live, ati mwambowu udzachitika m’chaka cha 2026 m’malo mwa chaka chino ku Cape Maclear m’boma la Mangochi.
Mkulu oyendetsa mwambowu, a Shadreck Kalukusa, ati adayika zaka ziwiri zokonzekera kuti phwandoli likhale lapamwamba.
“Tikufuna phwando lathu lidzifanana ndi mapwando a anzathu akunja. Taonani zimene anachita Chris Brown ku South Africa,” a Kulukusha anatero.
Iwo ati oyimba amene adzakhalepo pa mwambowo ndi akatswiri a m’dziko la Jamaica ndi mayiko ena, kotero akufuna kukhala ndi nthawi yokwanira yosonkhanitsa zipangizo ndi ndalama zokwanira.
“Pakadalipano, oyimba mmodzi watheka kale ndipo mwezi wamawa tilengeza mndandanda wa oyimbawa,” iye anatero.
Oyendetsa mwamboyu anali mmodzi mwa anthu amene anathandiziranso ulendo wa Burning Spear kudzaimba m’dziko lino kwa nthawi yoyamba.
Ku Mingoli Bash inayamba m’chaka cha 2023 ndi cholinga chotukula luso laoyimba ku Malawi.