Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Ntchito za GESD zakondweretsa anthu m’boma la Chiradzulu

Anthu a m’boma la Chiradzulu ati ndi okondwa kamba ka ntchito za chitukuko zosiyanasiyana zomwe zikuchitika kudzera mu thumba la ntchito za chitukuko laboma la GESD.

Mwachitsanzo, malo ophunzitsira achinyamata luso la ntchito zamanja a Mbulumbuzi Youth Development Centre ndi amodzi mwa malo amene apereka chiyembekezo kwa anthu m’bomali.

Malowa, omwe akupita kumapeto komaliza kumangidwa, adzidzaphunzitsira achinyamata luso monga kusoka, ukalipentala, kuotchelera zinthu mwazina.

Kudzera mu thumba la chitukuko cha bomali, khonsolo ya boma la Chiradzulu ikumanganso chipatala cha Chambe m’mudzi mwa Ntauchira, chomwe adzidzathandizirapo amayi oyembekezera komanso ana osapitilira zaka zisanu.

Ndipo a mfumu a Chanza ayamika boma kudzera mu thumba la chitukuko la GESD, kuti tsopano adzipeza thandizo pa chipatala mosavuta.

Ndipo kumbali ya mayendedwe kudzera ku ntchito za thumba GESD, khonsolo ya Chiradzulu ikumanganso mlatho wa Nazombe omwe unakokoloka ndi Namondwe wa Freddy, zomwe zichititse kuti mavuto amayendedwe achepe.

Mmodzi mwa akuluakulu ku khonsolo ya Chiradzulu wati khonsoloyi ikuchita zotheka kuti ntchito zonse zomangamanga ziyende mwandondomeko, zikhale zokhalitsa ndikupilira ku mavuto odza kamba ka kusintha kwa nyengo.

Ntchitozi zikuchitika ndi la ndalama zoposa K400 million.

Olemba: Mercy Zamawa

Related posts

Masewero a lero ndi masamu — Kayira

Romeo Umali

Imodzi mwa mbava zomwe zinaba K19M ayigwira

Rabson Kondowe

Apalasa kuchoka Lilongwe mpaka Blantyre pofuna kutolera K100 million

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.