Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati boma lionetsetsa kuti zipangizo za ulimi zotsika mtengo zifike mwamsanga m’madera amene sizinafikebe.
Dr Chakwera anena izi munzinda wa Lilongwe pa misonkhano yoyimayima yomema anthu kuti alembetse mu kaundula wa voti amene ali mkati.
Mtsogoleriyu anati boma lake libwezera m’chimake ntchito za ulimi popereka zipangizo zotsika mtengo kwa alimi mu nthawi yake, kupereka ngongole kuti atukulire ulimi wawo komanso kuonetsetsa kuti alimi akudyelera thukuta lawo powathandiza kupeza misika yabwino ya mbewu zawo.
Dr Chakwera anatinso cholinga chawo ndi chakuti aMalawi atukuke ndipo miyoyo yawo isinthe pokhala ndi chakudya chokwanira.
Iwo anapemphanso anthuwa kuti akalembetse mu kaundula kuti akavote ndicholinga chakuti athandizire nawo kukonza tsogolo la dziko lino.