Apolisi amanga anthu okwana 696 omwe akuwaganizira kuti apalamula milandu yosiyanasiyana mdziko muno.
Malinga ndi mneneri wa apolisi mdziko muno a Peter Kalaya, ntchitoyi aigwira masiku atatu kuyambira lachitatu sabata yatha.
A Kalaya atinso apeza katundu osiyanasiyana yemwe akumuganizira kuti ndiobedwa.
Katunduyu ndi monga galimoto ziwiri, zipangizo za magalimoto, mankhwala a mchipatala kudzanso zakudya zosavomerezeka ndi zina zambiri.
Malinga ndi a Kalaya, ntchitoyi yomwe aigwira ndi maiko monga Zimbabwe, South Africa, Zambia, Angola ndi ena, zithandiza kulimbikitsa maubale a kagwiridwe ka ntchito kabwino kudzanso kukhwimitsa chitetezo mu Africa.
Olemba : Ghwabupi Mwabungulu