Malawi Broadcasting Corporation
News Nkhani

Zikomo a Chakwera – Atero ophunzira pa MUBAS

Ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya Mubas, yomwe kale inkaziwika kuti Polytechnic, athokoza mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pokweza ndalama zomwe ophunzirawa amalandira mu nthawi yomwe akuchita maphunziro awo.

Ndalamazi zakwera kufika pa K560,000 pachaka kuchoka pa K350,000.

Aka ndikachiwiri kuti boma likweze ndalamayi pamene mu chaka cha 2022 inakwera kuchoka pa K200,000 kufika pa K350,000.

Malinga ndi kalata yochokera kwa mtsogoleri wa bungwe la ophunzirawa, a Gershom Nyirenda, izi zawonetsa kuti a Chakwera amamva zopempha za anthu ndipo amalabadira za anthu a m’dziko muno.

“A Chakwera mudziwe kuti ife ana ophunzira pa Mubas ndife othokoza kwambiri kamba ka utsogoleri wanu wamasomphenya owonetsetsa kuti maphunziro akupita patsogolo mdziko muno,” a Nyirenda atero.

Related posts

A CHAPONDA ALI PA MSONKHANO WINA NGATI WACHIWIRI KWA MTSOGOLERI WA DPP

MBC Online

Karonga United wins first home match against Mighty Tigers

Rabson Kondowe

Iranian President feared dead

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.