Apolisi ku Soche mumzinda wa Blantyre amanga Simple Jeputala wazaka 28 pomuganizira kuti anapha mlonda, Leyona Yona kenako ndikuba pamalo pomwe mlondayo amagwira ntchito.
Mneneri wapolisi ku Soche Aaron Chilala wati malemu Yona amagwira ntchito ku kampani yachitetezo ya Ichocho ndipo Jeputala nayenso anagwirapo ntchito ku kampani yachitetezo ya Ichocho koma anasiya ntchitoyo.
Patsikulo, malemu Yona amalondera pa malo osungira katundu a Anena Anena Logistics ndipo Jeputala analonderaponso pamalopo panthawi yomwe amagwira ntchito kwa Ichocho.
Kenako gulu la mbava, kuphatikizapo Jeputala linafika pamalopo usiku ndikumenya mlondayo. Munthu wina yemwe anapita pamalopo kukasiya katundu mmawa, ndiye anapeza thupi la mlondayo.
Pakadali pano, apolisi akufufuza komwe kuli amzake a Jeputala.