Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Nzika yaku Mozambique ayigwira itathyola ndikuba mnyumba

Apolisi m’chigawo chakummwera amanga Richard Herema  wazaka 42, yemwe kwawo ndi ku Mozambique, pomuganizira kuti iyeyo pamodzi ndi amzake,l anathyola nyumba ziwiri ndikuba ndalama zoposa K3 million komanso foni zam’manja kudera la Thornwood ku Mulanje.

Ofalitsankhani wapolisi ku Mulanje, Innocent Moses, wati Herema anali mgulu la mbava 40 zomwe zakhala zikuvutitsa mderalo.

Pakadali pano, apolisi akufufuza amzake a Herema omwe anathawa.

Herema amachokera mmudzi wa Mbizi, Mfumu yaikulu Nazombe ku Milanje m’dziko la Mozambique koma amakonza njinga zakapalasa zowonongeka kuno ku Malawi.

#MBCDigital
#Manthu

Related posts

SAPP-MALABO INTERVENTIONS ENDING MALNUTRITION IN CHILDREN

MBC Online

Chitipa farmers urged to adopt liquid organic fertiliser

MBC Online

Organisation moves to strengthen resilience in disaster-prone areas

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.