Oyimba Kennedy ‘Papkid’ Kadewere wati sikoyenera kuti anthu aulumali adzitengedwa ngati olephera m’dziko muno.
Iye wapemphanso a Malawi kuti adziyika chidwi pothandizana ndi anthu oterewa kuti azindikire za kuthekera kumene alinako.
Papkid wanena izi pamene wangotulutsa kumene nyimbo yake yotchedwa “kondwera” imene akuti wayimba ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo uthenga olimbikitsa anthu aulumali kuti asamadziyang’anire pansi komanso kukhala moyo omangodandaula poganiza kuti alibe tsogolo.
Katswiriyu wapemphanso a Malawi kuti adziyika chidwi pothandiza oyimba amene amayimba nyimbo zokhala ndi uthenga watanthauzo chifukwa nyimbo zotero zili ndi kuthekera kothandiza pachitukuko cha dziko.