Dera la mfumu yaikulu Chiseka m’boma la Lilongwe lakwanitsa kuchotsa ana okwana 169 ku mabanja a ana kuyambira mu chaka cha 2023 kufikira pano, adindo atero.
Oyang’anira achinyamata m’derali, a Chimwemwe Diliwo, ndi amene anena izi ku Lilongwe pa msokhano umene bungwe la ArtGlo likuchititsa m’bomali omwe ukulimbana ndi nkhanza zimene ana akukumana nazo.
Iwo ati nkhanza zosiyanasiyana zikuchepa mderalo kaamba ka upangiri wamphamvu.
Olemba: Lonjezo Msodoka