Sipikala wanyumba yamalamulo a Catherine Gotani Hara ati dziko lino litengerepo mwayi paubale omwe ulinawo ndi dziko la China popititsa patsogolo ntchito zamalonda.
A Hara anena izi ku Lilongwe kutsatira kubwera kwa wachiwiri wa sipikala wa nyumba ya malamulo yadziko la China, a Cai Dafeng.
Malinga ndi a Hara, nyumba yamalamulo ndiyodzipereka kukonza malamulo komanso kupanga ena amene angathandizire nkhani zamalonda m’dziko muno.
Pakali pano dziko la China, mwazina, likugula fodya komanso soya m’dziko muno, zomwe a Hara ati ndizothandiza kupititsa patsogolo chuma chadziko lino.
Mwazina, a Dafeng anayendera nyumba yamalamulo yadziko lino,imene inamangidwa ndithandizo lochoka kudziko la China.