Malawi Broadcasting Corporation
Development Health Local Local News

Tithandizane kulimbana ndi khansa ya chiberekero — Chiponda

Nduna yazaumoyo, a Khumbize Kandodo Chiponda, yatsindika kufunika kogwirana manja pa ntchito yolimbana ndi khansa ya khomo la chiberekero m’dziko muno.

Ndunayi yayakhula izi ku Lilongwe pa msonkhano okambira za matenda a khansa yokhudza khomo la chiberekero.

A Chiponda ati ndi zodandaulitsa kuti amayi oposa 3,000 pa chaka m’dziko muno akumwalira kamba ka nthendayi.

A Chiponda anaonjezera kuti unduna wa zaumoyo uonetsetsa kuti atsikana azaka za pakati pa 9 ndi 14 akulandira katemera wa HPV, yemwe amateteza ku nkhansayi kuonetsetsa kuti malo oyezera khansa ya khomo la chiberekero adzipezeka m’zipatala zonse za m’dziko muno.

Related posts

Chimwendo praises MCP unity ahead of 2025 elections

Romeo Umali

Govt. reaffirms no Malawian will die of hunger

Romeo Umali

SCT gives hope to Cyclone Freddy survivors in Nsanje

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.