Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

‘Tidziyamba ndife aMalawi kutsatsa malonda a dziko lathu’

Mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati dziko lino silikuchita bwino kwenikweni chifukwa choti timataya nthawi ndikufalitsa zinthu zoononga mbiri yathu m’malo mofalitsa zambiri zabwino zomwe zikuchitika m’dziko muno.

Dr Chakwera ati tidziyamba ndife aMalawi kuonetsera zinthu zabwino zimene zili m’dziko muno.

Iwo ayankhula izi pamwambo wotsegulira sabata ya msonkhano waulimi, zokopa alendo komanso migodi omwe ukuchitikira ku Bingu International Convention Centre mumzinda wa Lilongwe.

Dr Chakwera atsindika kufunika kolimbikira zokhazo zopindulitsa dziko monga ulimi wamakono, ntchito zamigodi komanso zokopa alendo.

Related posts

Amunjata kaamba koba zipangizo za ESCOM

Romeo Umali

‘Zitukuko zikufalikira ponseponse’

Rabson Kondowe

Boma lalimbikitsa ulimi

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.