Mwambo opereka malo kwa atsikana osewera mpira wa miyendo mutimu ya Scorchers wayamba ndi kupereka zikalata zaumwini kwa osewerawa ku unduna wa zamalo ku Lilongwe, komwe atsikanawa asonkhana limodzi ndi aphunzitsi awo.
Malinga ndi chikalata chomwe unduna wazamalo wawerenga pamwambowu, atsikanawa akuyembekezeka kupanga chitukuko pamalowa pasanadutse zaka ziwiri ndikuti akalephera kutero, boma lidzatenganso malowa.
Pamwambowu pali akuluakulu a ku unduna wa za malo, unduna wa zamasewero komanso akuluakulu a bungwe loyendetsa mpira wa miyendo m’dziko muno la Football Association of Malawi ndipo mlendo olemekezeka ndi Chikumbutso Mtumodzi, mlembi wamkulu oyang’anira ntchito zosiyanasiyana ku unduna wa zamasewero.