Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Olemba nkhani awalangiza kuti afalitse nkhani zokhudza matenda a nkhawa ndi muubongo

Mlembi wamkulu wa bungwe la Malawi Redcross Society, Chifundo Kalulu l, wapempha olemba nkhani kuti agwiritse ntchito ukadaulo wawo polemba nkhani zokhudza matenda a nkhawa komanso amuubongo.

Kalulu amalankhula izi m’boma la Salima pamkumano wa pa chaka wa bungwe la olemba nkhani am’chigawo chapakati la Bwaila Media Club.

Iwo ati atolankhani atha kuthandiza kuphunzitsa anthu za kuwopsya kwa matendawa komanso kufunika kopeza thandizo mwansanga.

“Nkhani ya matenda a nkhawa komanso amuubongo ndi yomwe ikuchititsa kuti chiwerengero cha anthu odzipha chikwere mdziko muno. Kotero ifeyo tikudalira olemba nkhani kuti mutenge uthenga wa mmene anthu angapewere komanso kusaka thandizo pamene akukumana ndi mavuto a muubongo.” Watero Kalulu.

Wapampando wa bungwe la Bwaila Media Club, Felix Washon, wati olemba nkhani m’dziko muno ndi odzipereka kulemba ndi kufalitsa nkhani zomwe zingathandizire kusintha miyoyo ya anthu m’dziko muno.

Related posts

Ma Drone awaulutsa

Romeo Umali

Raiply Volleyball sponsorship rises to K25 million

Rabson Kondowe

MACRA donates 15 computers to Blantyre Teachers’ College

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.