Malawi Broadcasting Corporation
Education Nkhani

Palibe mtsikana abwezedwe ku MUST chifukwa cha fizi — Prof. Malata

Wachiwiri kwa Chancellor wa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Science and Technology (MUST), Professor Address Malata, wati atsikana onse omwe anawasankhira ku sukuluyi ndipo analephera kuyamba maphunziro chifukwa cha kusowa kwa ndalama zolipilira sukulu apite akayambe chifukwa ndalama zapezeka.

Professor Malata auza MBC kuti zoti atsikana adzisiya sukulu chifukwa chosowa malipiro MUST siikupanga nawo.

Iwo anena izi pamene kampani ya Illovo Sugar Malawi imaperaka ndalama zokwana K250 million ku thumba lothandizira ophunzira osowa, makamaka atsikana.

Iwo ati padakali pano, kuthumbali kuli ndalama zokwana K400 million.

Related posts

“A Gotani – Hara ali ndi luntha potsogolera” — President Chakwera

Romeo Umali

‘Lekani kusala ndi kuchitira nkhanza anthu omwe ali khungu lachi alubino’

Rabson Kondowe

Muzilimbikira ngakhale mutakumana ndi mavuto — Sife

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.