Imodzi mwa matimu a mpira wa miyendo wa asungwana ya Ntopwa yati ena mwa osewera ake ayamba kutenga mimba zosayembekezera kamba koti akungokhala osasewera mpira kwa miyezi itatu tsopano.
Mkulu woyendetsa timu yi, Isaac Jomo Osman, wati kuyima kwa mpikisano wa asungwana kwapangitsa kuti osewera wa adzingokhala ndipo akumalowelera pochita zinthu zosayenera.
Mpikisano wa mpira wamiyendo wa asungwana m’dziko muno unayima kaye m’mwezi wa December chaka chatha pomwe nthambi yoyendetsa masewerowa ikudikilira ndalama kuchokera ku bungwe la FAM kuti amalizitse ndime ziwiri zomwe zatsala.
Mkulu woyendetsa mipikisano komanso kufalitsa nkhani ku bungwe la FAM, Gomezgani Zakazaka, anauza MBC kuti kuchuluka kwa ngongole zomwe bungweli linali nazo chaka chatha kunapangitsa kuti asinthe mndandanda wa kagwiritsidwe ntchito kwa ndalama zomwe, zina mwa izo, zinali zoyendetsera mpikisano wa asungwana wu.
Komabe a Zakazaka ati FAM ikuyesetsa kuti amalizitse mpikisano wa asungwanawu kuti akonzekere wa chaka chino.
Olemba: Amin Mussa
#MBCOnlineServices