Komiti yoona za chitetezo komanso ubale wa dziko lino ndi maiko ena yabweza ena mwa akuluakulu a nthambi yoona zolowa ndi kutuluka m’dziko muno kaamba ka kuti mkulu wa nthambiyi, a Brigadier General (Opuma) Charles Kalumo, sanali nawo mugulu limene lidayitanidwa kukaonekera ku komitiyi.
Mbali ziwirizi zimayenera kuti zikumane ndi kukambirana za m’mene ntchito yokonza ziphaso zolowera komanso kutulukira m’dziko muno ikuyendera.
Pofotokoza, wapampando wa komitiyi, a Patrick Siyabonga Bandawe, anati a Kalumo sanatsate ndondomeko yoyenera popeza iwo anangotchaya thenifolo kuwauza kuti sakwanitsa kufika ku mkumanowo.
A Bandawe anati izi ndi zobwezeretsa m’mbuyo chifukwa zimene amafuna akambirane ndi zofunika koposa kaamba kavuto limene dziko lino likukumana nalo popanga ziphatso.
Mu uthenga wa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, umene adapereka mu nyumba ya malamulo, iye adati ndiokhumudwa poona kuti ntchito yokonza ziphaso idayima chifukwa cha anthu ena osokoneza amene adalowelera makina osindikizira ziphasozi ndipo akufuna ndalama kuti ntchitoyi iyambenso.
Nduna yoona za chitetezo cha m’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, adati zigawengazi zikufuna ndalama yokwana K 2 Billion, zomwe boma silingayelekeze kupereka.
Ndipo bungwe la akatswiri pa makina a Kompyuta m’dziko muno la ICTAM lidati ligwira ntchito ndi boma pofuna kuthana ndi akathyaliwa ndi kubwezeretsa ntchitoyi m’chimake.
Pamene izi zikuchitika, a chinyamata ambiri akhala akudandaula chifukwa akulephera kupeza ziphasozi kuti apite m’dziko la Israel akagwire ntchito.