Boma lati anthu amene ayamba kulandira ndalama za mtukula pakhomo akhale ndi dongosolo la kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo pofuna kuti miyoyo yawo itukuke ntchitoyi ikamatha.
Mlembi wamkulu mu unduna oona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi, Dr Nertha Semphere Mgala, amayankhula izi pa bwalo la milandu la kwa mfumu Chimaliro m’boma la Thyolo pamene amadzayendera m’mene ntchitoyi yayambira.
Chiyambireni mwezi watha, mabanja opyola 14,000 ndi amene akuyenera kuti alandire ndalama yokwana K150,000 kamodzi mwezi uno kuti agulire chakudya.
Ndalamazi zikumafikira mu lamya zawo za m’manja zomwe anadzilembetsa pa netiweki ya TNM.
Ndipo adindo ku unduna oona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi apempha kampani ya TNM kuti isamatseke ma nambala a anthu omwe akulandira Mtukula Pakhomo chifukwa sakugula ma unitsi.
Zimenezi, adindo a kampaniyo anavomereza ndipo anatsimikiza kuti zokambilana zili mkati pofuna kukonza mavuto onse okhudza nambala zawo omwe anthu akukumana nawo mu ndondomekoyi.
Maboma oposa khumi ndi amene ali m’ndondomeko yatsopanoyi.
Olemba: Naomi Kamuyango