Nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda ati unduna wao uonetsetsa kuti wapereka ndalama zokwanila ku bungwe la NEEF.
Poyankhula pomwe akuyendela ntchito za NEEF m’maboma osiyanasiyana kuona momwe anthu akupindulila ndi ngongole za NEEF, a Chithyola-Banda ati pomwe aphungu adzikumana kuyambila pa 9 February mwezi uno, akaonetsetsa kuti akambilane mozama nkhani yokhudza bungwe la NEEF lomwe ati ndalama zake zikupindulila madera onse komwe kuli aphungu.
M’mau ake nduna yazofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, ati boma la Prezidenti Dr Lazarus Chakwera likuchita chilichonse chotheka poonetsetsa kuti mdziko muno muli chakudya chokwanila nthawi zonse.
M’mau ake membala wa komiti yaikulu yoyendetsa ntchito za bungwe la NEEF a Jacob Mderu apempha anthu kuti apitilize kubweza ngongole ncholinga choti anthu ambili apindule mdziko muno.
Bungwe la NEEF analipatsa K75 billion kuti lipereke ngongole koma panopa linadutsa kale kufika pa K87 billion.
Magulu kapena munthu m’modzi mdziko muno amatha kutenga ngongole kuyambila K1 million kapena kuposera pamenepo.
Wolemba Mayeso Chikhadzula.