Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ntchito yomanga nsewu wa Manja yakondweresa anthu

Anthu okhala dera la Manja mu mnzinda wa Blantyre ati ndiokondwa ndi ganizo la boma lofuna kuyamba ntchito yomanga nsewu kuderali.

Boma kudzera ku khonsolo ya mu mnzinda wa Blantyre likufuna kumanga nsewuwu ndi ndalama zokwana K2.6 billion ndipo kampani ya zomangamanga ya DEC ndiyomwe imange nsewu-wu

Anthu okhala ku Manja ati tsopano ndi okondwa kuti boma layankha pempho lawo patapita zaka zambiri akuvutika.

“Pafupifupi aliyense kudera lino ali ndi galimoto ndipo nsewu-wu umationongera galimoto zathu. Tamva kuti ntchito yomanga nsewu-wu ikuyamba pompano ndipo ndife okondwa” Anatero Mayi Florence Chirambo, m’modzi mwa anthu okhala kuderali.

Kwa nthawi yaitali anthu okhala dera la Manja akhala akudandaula chifukwa cha vuto la nsewu.

Related posts

Karonga United, Moyale Barracks proceed to FDH Cup Semi-Final

Romeo Umali

National Bank yapanga phindu lokwana K71.96 billion chaka chatha

Alinafe Mlamba

ADL to construct Airport City

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.