Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati pakufunika m’gwirizano wa mphamvu pakati pa bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) ndi mabungwe amene amagwira nawo ntchito pofuna kuti ntchito zofalitsa uthenga zipite patsogolo.
A Kunkuyu amafotokoza izi mu mzinda wa Blantyre pamene amatsegulira msonkhano wa sabata imodzi wa bungwe la MACRA ndi ma bungwe amene amagwira nawo ntchito.
Iwo anati zikatere zipereka danga kwa ma bungwe komanso kuti amvetsetse ntchito za MACRA komanso m’mene angagwilire ntchito limodzi pofuna kukweza luso lofalitsa ma uthenga pogwiritsa ntchito zipangizo za makono.
Mkulu wa bungwe la MACRA, a Daud Suleman, anati dziko la Malawi likhazikitsa malamulo atsopano omwe azitsogolera momwe mabungwe komanso anthu azigwiritsira ntchito zipangizo maiuthenga mogwirizana ndi luso la makono.
Mwambo ngati omwewu ukhalaponso m’mizinda ya Lilongwe ndi Mzuzu.