Nthambi yowona za nyengo yati tsopano palibe chiwopsezo choti namondwe aliyense atha kufika m’dziko muno.
Masiku apitawa, nthambiyi inalengeza kuti namondwe atha kubadwa pa nyanja ya mchere ya India lamulungu pa 10 March 2024.
Koma mu lipoti la posachedwapa, nthambiyi inatsimikiza kuti namondweyu sangakhalepo koma ngati angabadwe, mwayi ofika ku Malawi ndi ochepa zedi.
M’neneri wawo, Yobu Kachiwanda, anangoti pakadali pano anthu ayembekezere mitambo, mphepo ndi mvula m’ma boma ena akum’mwera.
A Kachiwanda anachenjezanso a Malawi kuti akhale a tcheru potsatira nkhani za nyengo.
Olemba : Blessings Cheleuka