Mtsogoleri wa dziko la America, a Donald Trump, ayamikira mayiko a Israel ndi Iran kaamba koonetsa chidwi chothetsa nkhondo, malinga ndi nyumba youlutsa mawu ya BBC.
Izi zilichomwechi pamene dziko la Iran linaponya mizinga kumalo a asilikali a America m’dziko la Qatar ngati kubwezera zimene dziko la America ndi Israel anachita posakaza malo a nuclear ku Iran.
Pakadalipano, Israel yavomera kuleka kumenya nkhondo ndi Iran.
M’mawu ake, nduna yoona nkhani za kunja kwa dziko la Iran, a Seyed Araghchi, ati dziko lawo lichita chimodzimodzi ngati Israel itasiya kuchitira chiwembu dziko lawo.
Olemba: Telson Magombo